Mawu a M'munsi
a Pa Masada, akatswiri ofukula zofotseredwa m’mabwinja anapeza ndalama mazanamazana zokhala ndi malembo ozokotedwa Achihebri okondwerera kupandukako, monga ngati “Za Ufulu wa Ziyoni” ndi “Yerusalemu Woyera.” Dr. Yigael Yadin m’bukhu lake lakuti Masada akulongosola motere: “Masekeli amene tinawapeza onse amasonyeza kupanduka kwa zaka zonsezo, kuyambira chaka choyamba mpaka chaka chosadziŵika kwambiri chachisanu, chaka chomalizira chimene sekeliyo inasulidwa, chimagwirizana ndi chaka cha 70 AD pamene Kachisi wa Yerusalemu anawonongedwa.” Onani ndalama ili pamwambayo.