Mawu a M'munsi
a NthaƔi zina atsogoleri achipembedzo eniwo anakhala asilikali. Pa Nkhondo ya Hastings (1066), bishopu Wachikatolika wotchedwa Odo analungamitsa kudziloƔetsa kwake kokangalika mwa kugwiritsira ntchito chibonga mmalo mwa lupanga. Iye ananena kuti ngati mwazi sunakhetsedwe, munthu wa Mulungu akhoza kupha movomerezedwa ndi lamulo. Zaka mazana asanu pambuyo pake, Kadinala Ximenes mwiniyo anatsogolera kuukiridwa kwa North Africa kochitidwa ndi Spain.