Mawu a M'munsi
a M’Malemba Achihebri monse, amuna ndi akazi a mu ukwati kaŵirikaŵiri amatchedwa monga “mwamuna” (Chihebri, ʼish) ndi “mkazi” (Chihebri, ʼish·shahʹ). Mwachitsanzo, mu Edene, mawu amene Yehova anagwiritsira ntchito anali, osati “mwini” ndi ‘wa mwini,’ koma “mwamuna” ndi “mkazi.” (Genesis 2:24; 3:16, 17) Ulosi wa Hoseya unaneneratu kuti atabwerako ku ukapolo, Israyeli molapa akatcha Yehova kuti “Mwamuna wanga,” ndipo osatinso ‘mwini wake wa ine.’ Zimene zikupereka lingaliro lakuti liwulo “mwamuna” linali lopereka lingaliro lachikondi kwambiri kuposa lakuti “mwini.”—Hoseya 2:16.