Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO

Mawu a M'munsi

a Akristu ena ogwira ntchito m’chipatala afika polingalira mfundo imeneyi yaulamuliro. Dokotala angakhale ndi ulamuliro wolamula mankhwala kapena chinthu choyenera kuchitidwa pa wodwala. Ngakhale kuti wodwalayo sangakane, kodi dokotala wachikristu wokhala ndi ulamulirowo angalamule bwanji kuti aikidwe magazi kapena kuchotsa mimba, akudziŵa zimene Baibulo limanena pa nkhani zimenezi? Mosiyana ndi zimenezo, nesi wolembedwa ntchito m’chipatala angakhale alibe ulamuliro umenewo. Pochita ntchito zake za masiku onse, dokotala angamuuze kuti ayese magazi a wodwala pa zolinga zina kapena kuti asamalire wodwala amene wabwera kudzachotsa mimba. Mogwirizana ndi chitsanzo cholembedwa pa 2 Mafumu 5:17-19, atha kuona kuti popeza iye alibe ulamuliro umenewo ndipo sindiye walamula kuti wodwala aikidwe magazi kapena kuchotsa mimba, iye angapereke thandizo wamba kwa wodwalayo. Zoonadi, adzayenerabe kuganizira chikumbumtima chake, kuti ‘akhale pamaso pa Mulungu ndi chikumbumtima chokoma.’​—Machitidwe 23:1.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena