Mawu a M'munsi
a Monga momwe Yesu anavumbulira m’fanizo la tirigu ndi namsongole ndi m’fanizo lake la njira yotakata ndi yopapatiza (Mateyu 7:13, 14), Chikristu choona chinali kudzapitirizabe ndi anthu ochepa m’mibadwo yonse. Komabe, anthuwo sanali kudzaonekera kwambiri chifukwa cha kuchulukitsitsa kwa anthu onga namsongole, amene anali kudzadzionetsera okha ndi ziphunzitso zawo monga nkhope yeniyeni ya Chikristu. Imeneyi ndiyo nkhope imene nkhani yathu ikunena.