Mawu a M'munsi
b Mawu akuti “helo” amatembenuzidwa ku mawu achihebri akuti Sheol ndi mawu achigiriki akuti Hades, ndipo onse aŵiri amangotanthauza “manda.” Chotero, pamene kuli kwakuti amene anatembenuza Baibulo lachingelezi la King James Version anatembenuza Sheol nthaŵi 31 kukhala “helo,” anatembenuzanso mawu omwewo nthaŵi 31 monga “manda” ndiponso katatu monga “dzenje,” zomwe zikusonyeza kuti mawu ameneŵa amatanthauzadi chinthu chimodzimodzi.