Mawu a M'munsi
a Buku la Insight on the Scriptures, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc., limalongosola kuti: “Malinga ndi mmene amagwiritsidwira ntchito m’Baibulo, mawu akuti ‘chotetezera’ ali ndi lingaliro lalikulu la ‘kuphimba’ kapena ‘kusinthanitsa,’ ndipo chimene chikuperekedwa posinthanitsapo, kapena monga ‘chophimba’ cha, chinthu chinanso chiyenera kukhala chofanana nacho ndendende. . . . Kuti pakhale chotetezera chokwanira cha chimene chinatayidwa ndi Adamu, nsembe yauchimo yokhala ndi mtengo wofanana ndendende ndi moyo wa munthu wangwiro inafunika kuperekedwa.”