Mawu a M'munsi
a Nkhani inanso siyenera kunyalanyazidwa: Pa mwambo wa nacimiento ku Mexico, mwanayo amatchulidwa kuti “Mulungu Mwana” chifukwa cha malingaliro akuti anali Mulungu mwiniyo yemwe anabwera padziko lapansi monga khanda. Koma Baibulo limalongosola Yesu kukhala Mwana wa Mulungu yemwe anadzabadwa padziko lapansi; sanali Mulungu mwiniyo kapena wolingana ndi Yehova, Mulungu wamphamvuyonse. Talingalirani za zoona zake za nkhani imeneyi, zomwe zafotokozedwa pa Luka 1:35; Yohane 3:16; 5:37; 14:1, 6, 9, 28; 17:1, 3; 20:17.