Mawu a M'munsi
a Zolembedwa za Apocrypha (kutanthauza “zobisika”) ndiponso Pseudepigrapha (kutanthauza “zolembedwa zonamizira kulembedwa ndi anthu ena”) n’zolembedwa zachiyuda zoyambira m’zaka za zana lachitatu B.C.E. mpaka m’zaka za zana loyamba C.E. Tchalitchi cha Roma Katolika chimavomereza zolembedwa za Apocrypha kukhala mbali ya mabuku ouziridwa a m’Baibulo, koma Ayuda ndi Apulotesitanti sawavomereza mabuku ameneŵa. Zolembedwa za Pseudepigrapha nthaŵi zambiri zimakhala ngati kuti zikupitiriza nkhani za m’Baibulo, zolembedwa m’dzina la munthu wina wa m’Baibulo wodziŵika bwino.