Mawu a M'munsi
b Dzina lakuti “Chisilavo,” limene lagwiritsidwa ntchito m’nkhani ino, likusonyeza chinenero cha Asilavo chomwe Cyril ndi Methodius ankalankhula pa ntchito yawo ndiponso chomwe anagwiritsa ntchito m’zolemba zawo. Ena lerolino amagwiritsa ntchito mawu akuti “Chisilavo Chakale” kapena “Chisilavo Chakale cha Tchalitchi.” Akatswiri a zinenero amavomereza kuti m’zaka za zana la chisanu ndi chinayi C.E., panali zinenero zambiri zomwe Asilavo ankalankhula.