Mawu a M'munsi
a Ngakhale kuti tsopano mtsinje wa Firate umadutsa pamtunda wa makilomita pafupifupi 16 kum’maŵa kwa malo omwe kale panali mzinda wa Uri, umboni ukusonyeza kuti kalelo mtsinjewo unkadutsa pafupi kwambiri chakumadzulo kwa mzindawo. N’chifukwa chake Abramu ankati anali wochokera “tsidya lija la mtsinje [wa Firate].”—Yoswa 24:3.