Mawu a M'munsi
a Wophunzira Stefano anafotokozanso mfundo zina zimene sizikupezeka paliponse m’Malemba Achihebri. Anafotokoza za kuphunzira kwa Mose nzeru zonse za Aigupto, zoti anali ndi zaka 40 pothaŵa ku Igupto, zoti anakhala ku Midyani kwa zaka 40, ndiponso zoti angelo anatenga nawo mbali popereka Chilamulo cha Mose.—Machitidwe 7:22, 23, 30, 38.