Mawu a M'munsi
b Pamsonkhano wa bungwe la zipembedzo lakuti United States International Religious Freedom Commission pa November 16, 2000, mmodzi mwa anthu amene analipo anasiyanitsa anthu amene amatembenuza anthu moumiriza ndi ntchito ya Mboni za Yehova. Ananena kuti, Mboni za Yehova zikamalalikira kwa ena, zimatero mwa njira yakuti munthu atha kungoyankha kuti “sindifuna kumva uthenga wanu” n’kutseka chitseko.