Mawu a M'munsi
a Mefiboseti yemwe anali woyamikira ndiponso wodzichepetsa sakanakhala ndi maganizo ofuna kulanda ufumu motero. Mosakayika, iye ankadziŵa za kukhulupirika kwa atate wake, Yonatani. Ngakhale kuti anali mwana wa Mfumu Sauli, Yonatani anazindikira modzichepetsa kuti Davide ndi amene Yehova anam’sankha kuti adzakhale mfumu ya Israyeli. (1 Samueli 20:12-17) Yonatani, monga kholo loopa Mulungu la Mefiboseti ndiponso bwenzi lokhulupirika la Davide, sakanaphunzitsa mwana wake kuti azilakalaka kutenga ufumu.