Mawu a M'munsi
a “Nyenyezi” panopa sizikuimira angelo enieni. Yesu sangagwiritse ntchito munthu kulembera uthenga zolengedwa zauzimu zosaoneka. Motero, “nyenyezi” zikuimira oyang’anira aumunthu, kapena akulu, m’mipingo, amene ali monga amithenga a Yesu. Chiŵerengero chawocho, asanu ndi aŵiri, chikutanthauza kukwanira malinga ndi muyezo wa Mulungu.