Mawu a M'munsi
a Ankatchedwa Awadensi chifukwa cha Pierre Vaudès, kapena kuti Peter Waldo, mkulu wina wamalonda wa m’zaka za m’ma 1100 mu mzinda wa Lyons, ku France. Waldo anachotsedwa m’Tchalitchi cha Katolika chifukwa cha zikhulupiriro zake. Kuti mudziŵe zochuluka pankhani ya Awadensi, onani nkhani yakuti “Awadensi—Gulu la Mpatuko Lomwe Linaloŵa Chipulotesitanti” mu Nsanja ya Olonda ya March 15, 2002.