Mawu a M'munsi
a M’Baibulo la King James Version liwu lachigiriki lakuti Hade analimasulira kuti “helo” m’malo khumi omwe liwuli limapezeka m’Malemba Achigiriki Achikristu. Pa Luka 16:19-31 pamatchula za malo a mazunzo, koma nkhani yonseyo ndi yophiphiritsa. Onani chaputala 88 cha buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.