Mawu a M'munsi
a Yesu anagwiritsa ntchito mafanizo osiyanasiyana, ena mwa iwo anali zitsanzo, mafanizo oyerekezera chinthu china ndi chinzake, ndiponso mafanizo ofananitsa. Koma iye amatchuka n’kugwiritsa ntchito kwambiri mafanizo osimba nthano, omwe ndi “nkhani yaifupi, nthaŵi zambiri yopeka, imene munthu angaphunzirepo makhalidwe abwino kapena choonadi chauzimu.”