Mawu a M'munsi
a Buku la Tobit, limene liyenera kuti analilemba m’zaka za m’ma 200 B.C.E., muli nkhani yodzala ndi kukhulupirira malodza ya Myuda wina dzina lake Tobias. Iye anam’nena kuti ankatha kupeza mphamvu zochiritsa ndi kutulutsa ziŵanda pogwiritsa ntchito mtima, ndulu, ndi chiwindi cha chinsomba chachikulu kwambiri.