Mawu a M'munsi
a Nehemiya 3:5 akufotokoza kuti Ayuda ena otchuka, anthu “omveka,” anakana kugwira nawo ntchitoyo, koma ndi okhawo amene anatero. Anthu osiyanasiyana, kaya ansembe, osula golidi, osanganiza zonunkhira, akulu a madera, ndiponso amalonda, anathandiza nawo ntchitoyi.—Mavesi 1, 8, 9, 32.