Mawu a M'munsi
a N’zokayikitsa kuti mumzinda wa Yerusalemu munali anthu oposa 120,000 m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino. Eusebius anaŵerengetsera kuti anthu 300,000 a m’chigawo cha Yudeya anapita ku Yerusalemu kukachita phwando la Paskha mu 70 C.E. Anthu ena amene anaphedwawo ayenera kuti anachokera m’madera ena a mu ufumuwo.