Mawu a M'munsi
a Ichi n’chifukwa china chimene anthu a ku Armenia akamaganiza za phiri la Ararati amangoona ngati lili m’dziko lawo. Kale, Armenia unali ufumu waukulu umene unkafika mpaka ku mapiri ameneŵa. N’chifukwa chake pa Yesaya 37:38, Baibulo lachigiriki la Septuagint, m’malo molemba kuti “dziko la ku Ararati” linangoti “Armenia.” Masiku ano phiri la Ararati lili m’dziko la Turkey, kufupi ndi malire ake a kummaŵa.