Mawu a M'munsi
b Nkhaŵa imene aifotokoza panoyi akuti ndiyo “nkhaŵa yobwera chifukwa cha mantha, imene imamuchotsera munthu chimwemwe chonse.” Kunena kuti “musadere nkhaŵa” kukukhala ngati zikutanthauza kuti sitiyenera kuyamba kuda nkhaŵa. Koma buku lina laumboni limati: “Verebu la Chigirikilo ndi lamulo losonyeza kuti zinthuzo zichitike nthaŵi yomwe ino, kusonyeza kulamula kuti munthu asiye kuchita chinachake chimene wayamba kale kuchichita.”