Mawu a M'munsi
d Magazini ofotokoza za m’Baibulo ameneŵa salimbikitsa mankhwala a mtundu wina uliwonse chifukwa imeneyi ndi nkhani imene munthu amasankha yekha chochita. M’malo mwake, cholinga cha nkhanizi n’kudziŵitsa anthu amene amaŵerenga magaziniwa mfundo zokhudza matendawo malinga ndi mmene anthu akuzidziŵira pakalipano.