Mawu a M'munsi
a M’chipululu, Aisrayeli ndiponso “anthu ambiri [osakanizika, NW]” anafunika kudya mana kuti akhale ndi moyo. (Eksodo 12:37, 38; 16:13-18) Momwemonso, Akristu onse, kaya ndi odzozedwa kapena ayi, kuti akhale ndi moyo wosatha ayenera kudya mana a kumwamba mwa kukhulupirira mphamvu zopulumutsa za thupi ndi mwazi wa Yesu zomwe zinaperekedwa nsembe.—Onani Nsanja ya Olonda, ya February 1, 1988, masamba 30 mpaka 31.