Mawu a M'munsi
b Ngakhale kuti Akristu oona amadziŵa kuti ulamuliro wa anthu nthaŵi zambiri umakhala ngati chilombo, iwo amagonjera “maulamuliro aakulu” a maboma malinga ndi malangizo a m’Baibulo. (Aroma 13:1) Koma maulamuliro ameneŵa akalamula Akristuwo kuchita zinthu zotsutsana ndi lamulo la Mulungu, iwo ‘amamvera Mulungu koposa anthu.’—Machitidwe 5:29.