Mawu a M'munsi
a M’Malemba, mawu akuti “chidani” ali ndi matanthauzo angapo. Nthaŵi zina, amangotanthauza kusakonda kwambiri chinthu chinachake. (Deuteronomo 21:15, 16) Mawu akuti “chidani” nthaŵi zina amatanthauzanso kuipidwa kwambiri ndi chinthu chinachake popanda maganizo alionse ochiwononga, koma n’kumachipeŵa chifukwa chonyansidwa nacho. Koma mawu akuti “chidani” angatanthauzenso kuipidwa kwambiri ndiponso kwa nthaŵi yaitali ndi chinthu chinachake ndipo nthaŵi zambiri kophatikiza ndi dumbo. Ndi chidani chamtundu umenewu chimene tifotokoze m’nkhaniyi.