Mawu a M'munsi
a Mfundo zomwe zatchulidwa m’ndime ino ndi ndime yotsatira zikusonyeza miyambo ya kumayiko kwina kumene banja la mtsikana limayenera kupereka katundu kapena mphatso ku banja la mwamuna. M’mayiko ambiri ku Africa kuno mwamuna kapena banja lake ndi amene amayenera kupereka malowolo ndi mphatso ku banja la mtsikana. Komabe mfundo zimene zatchulidwazo zikukhudza miyambo iŵiri yonseyi.