Mawu a M'munsi
a Buku lotchedwa La Sagrada Escritura y comentario por profesores de la Compañía de Jesús (Malemba Opatulika, Nkhani ndi Ndemanga Zolembedwa ndi Gulu la Aphunzitsi a Chipani cha Yesu) limafotokoza kuti “pakati pa Aperisi, Amedi ndi Akasidi, Anzeru a kum’mawa ndiwo anali gulu la ansembe amene ankalimbikitsa maphunziro a zamatsenga, kupenda nyenyezi komanso mankhwala.” Komabe, pofika m’zaka za m’ma 500 mpaka 1500 C.E, gulu la Anzeru a kum’mawa amene anabwera kudzaona Yesu ali mwana, anayamba kutchedwa kuti oyera ndipo anapatsidwa mayina akuti: Melchior, Gaspar, ndi Balthasar. Ndipo mafupa awo akuti amasungidwa mu tchalitchi chachikulu cha mu mzinda wa Cologne, ku Germany.