Mawu a M'munsi
a Katswiri wina wolemba ndakatulo wachiroma, dzina lake Horace (yemwe anabadwa mu 65 ndi kumwalira m’chaka cha 8 B.C.E), amene anadutsapo msewu umenewo, anafotokozapo mavuto omwe anthu ankakumana nawo chakumapeto kwa ulendo wodutsa msewu umenewu. Horace ananena kuti Bwalo la Apiyo, lomwe kwenikweni linali msika, linali “lodzaza ndi oyendetsa mabwato ndiponso anthu oumira kwambiri omwe anali ndi nyumba za alendo.” Iye anadandaula za “tizilombo touluka toluma kwambiri ndiponso achule osowetsa mtendere” komanso za madzi ake “owawa.”