Mawu a M'munsi
c Pa sayansi, n’kulakwitsa kunena kuti dzuwa “limatuluka” ndiponso “limalowa.” Koma sikulakwa kunena choncho polankhulana tsiku ndi tsiku, chifukwa ndi mmene dzuwa limaonekera tikakhala padziko pano. Moteronso, Yoswa sikuti anali kunena za sayansi ya zakuthambo, koma ankangosimba zimene zinachitikazo mogwirizana ndi mmene iyeyo anazionera.