Mawu a M'munsi
b Iye anali wodziwa bwino Chiarabu, Chigiriki, Chihebri, Chilatini, ndi Chisuriya. Izi ndizo zinali zinenero zikuluzikulu zisanu zimene zinagwiritsidwa ntchito polemba Baibulo Lophatikiza Zinenero limeneli. Analinso katswiri pa zinthu zakale zofukulidwa pansi, komanso pa zamankhwala, zachilengedwe, ndi zaumulungu. Maphunziro ake pambali zimenezi anam’thandiza kwambiri pokonza nkhani zakumapeto kwa Baibulo limenelo.