Mawu a M'munsi
a Mlongo Morgou anabwerera ku France ndipo anatha kukonza ulendo wachisanu wa ku Togo, womwe anapita pa October 6, 2003, n’kubwerera kwawo pa February 6, 2004. N’zomvetsa chisoni kuti chifukwa cha thanzi lake, n’kutheka kuti umenewu unali ulendo wake wotsiriza wa ku Togo m’dongosolo lino la zinthu. Komabe, cholinga chake chachikulu chidakali chotumikira Yehova.