Mawu a M'munsi
b Mofanana ndi zimenezi, pofotokoza za ubale watsopano wa pakati pa Mulungu ndi “ana” ake odzozedwa ndi mzimu, Paulo anagwiritsa ntchito mfundo ya zamalamulo yomwe inali yodziwika kwa anthu a mu Ufumu wa Roma omwe anawerenga kalata yake. (Aroma 8:14-17) Buku lakuti St. Paul at Rome limati: “Aroma, pachikhalidwe chawo, ankatha kutenga mwana wa wina n’kumulera kukhala wawo, ndipo umenewu ndiwo unali mchitidwe wofala m’mabanja a Aroma.”