Mawu a M'munsi
a Dziko lapansi, Mercury, Venus ndi Mars ndiwo mapulaneti anayi oyandikana kwambiri ndi dzuwa lathu. Mapulaneti amenewa ali ndi nthaka ndi miyala. Koma mapulaneti aakulu okhala kutali ndi dzuwa lathu otchedwa Jupiter, Saturn, Uranus, ndi Neptune, n’ngopangidwa makamaka ndi mpweya.