Mawu a M'munsi
a Kuyambira cha m’ma 1550, tchalitchi cha Katolika chinatulutsa ndandanda ya mabuku oletsedwa (Index of Forbidden Books), n’kuletseratu kugwiritsa ntchito Mabaibulo a zinenero wamba. Buku lina (The New Encyclopædia Britannica) linati, “kwa zaka 200, zimenezi zinaimitsiratu ntchito yomasulira ya tchalitchi cha Katolika.”