Mawu a M'munsi
a Malemba amagwiritsa ntchito mawu akuti “kuwala” m’njira zosiyanasiyana zophiphiritsa. Mwachitsanzo, Baibulo limati Mulungu ndi kuwala. (Salmo 104:1, 2; 1 Yohane 1:5) Ndiponso limayerekezera kuwala ndi mfundo zonena za Mulungu zopezeka m’Mawu ake. (Yesaya 2:3-5; 2 Akorinto 4:6) Pa utumiki wake padziko lapansi, Yesu anali kuwala. (Yohane 8:12; 9:5; 12:35) Ndipo otsatira a Yesu analamulidwa kuti aonetse kuwala kwawo.—Mateyo 5:14, 16.