Mawu a M'munsi
a Mofanana ndi zimenezi, Owen Gingerich, katswiri wa zakuthambo wa pa yunivesite ya Harvard, analemba kuti: “Mtima wosadzikonda ungatichititse kufunsa funso limene . . . asayansi sangaliyankhe mwa kungophunzira za nyama. Yankho logwira mtima lingapezeke mwa kuphunzira zinthu zina ndipo lingakhudze makhalidwe amene Mulungu anapatsa anthu, kuphatikizapo chikumbumtima.”