Mawu a M'munsi
a Mofanana ndi pemphero lachitsanzo la Yesu, pemphero la pamaliro lachiyudali limanenanso kuti dzina la Mulungu liyeretsedwe. Ngakhale kuti pali kusiyana maganizo pankhani yoti pempheroli linayamba mu nthawi ya Khristu kapena n’lakale kwambiri kuposa nthawi imeneyi, koma sitiyenera kudabwa kuti mbali zina za mapempherowa zikufanana. Yesu sanapereke pemphero lake lija ndi cholinga chakuti aphunzitse mfundo zatsopano. Mfundo iliyonse ya m’pempheroli inali yogwirizana kwambiri ndi Malemba amene Ayuda onse anali nawo panthawiyo. Yesu ankalimbikitsa Ayuda anzake kupempha zinthu zimene iwo ankapempha nthawi zonse.