Mawu a M'munsi
a Nkhani yonse imene Yakobe anali kufotokoza imasonyeza kuti iye polemba, anali kuganiza makamaka za akulu, kapena kuti “aphunzitsi” mumpingo. (Yak. 3:1) Inde, amuna amenewa ayenera kupereka chitsanzo chabwino chakuti ali ndi nzeru yeniyeni. Ngakhale ndi choncho, tonsefe tingapindule ndi uphungu wake.