Mawu a M'munsi
a M’mipukutu yodalirika ya Baibulo mulibe vesi 44 ndi 46. Akatswiri amavomereza kuti mavesi awiriwa anangowonjezeredwa pambuyo pake. Pulofesa Archibald T. Robertson analemba kuti: “M’mipukutu yakale kwambiri komanso yodalirika mulibe mavesi awiriwa. Mavesiwa anachokera m’mipukutu ya Kumadzulo ndi ya ku Suriya (Byzantine). Ndipo amangobwereza mawu a m’vesi 48. Choncho, m’mavesi athu [tachotsamo] vesi 44 ndi 46 amene si oona.”