Mawu a M'munsi
a Lemba la Akolose 3:9, 10 limasonyeza kuti mawu akuti tinalengedwa m’chifanizo cha Mulungu amatanthauza kuti tili ndi makhalidwe ofanana ndi a Mulungu. Anthu amene akufuna kukondweretsa Mulungu amalimbikitsidwa kuti avale “umunthu watsopano,” umene “ukukhalitsidwa watsopano, kukhala wogwirizana ndi chifaniziro cha [Mulungu] amene anaulenga.”