Mawu a M'munsi
a Taonani kusiyana kwa mawu a m’lembali ndi mawu ofotokoza ulendo wa Mariya wa m’mbuyomo. Ponena za ulendo wa m’mbuyomo, Malemba amati: “Mariya ananyamuka . . . ndi kupita” kwa Elizabeti. (Luka 1:39) Panthawiyi Mariya sanam’funse kaye Yosefe, chifukwa anali atangotomerana, motero anangonyamuka. Komano atakwatiwa, Yosefe ndi amene akutchulidwa ngati mwini wa ulendowo, osati Mariya.