Mawu a M'munsi
a Yesu ananena kuti: “Chifukwa chake khalani angwiro, monga Atate wanu wa kumwamba ali wangwiro.” (Mat. 5:48) Iye ankadziwa kuti ngakhale anthu opanda ungwiro angathe kuchita zinthu zabwino. Tingathe kusangalatsa Mulungu pomvera lamulo loti tizikonda anzathu ndi mtima wonse. Yehova ndi amene ali ndi ungwiro wosayerekezeka. Malemba akamanena za “umphumphu” wake amatanthauza kuti iye ndi wangwiro.—Sal. 18:30.