Mawu a M'munsi
c Panthawi imene Yesu ankayamba utumiki wake, Yosefe ayenera kuti anali atamwaliradi, chifukwa mabuku a uthenga wabwino amangotchula za amayi, ang’ono, ndi alongo ake a Yesu okha basi. Mwachitsanzo, paukwati wa ku Kana, Mariya analipo ndipo ankagwira nawo ntchito zina, koma palibe umboni uliwonse wosonyeza kuti Yosefe analipo. (Yohane 2:1-11 ) M’nkhani ina, anthu a m’tawuni ya kwawo kwa Khristu sanatchule Yesu kuti ndi mwana wa Yosefe, koma anamutchula kuti “mwana wa Mariya.”—Maliko 6:3.