Mawu a M'munsi
a Mawu amenewa amanena za mwambo winawake umene anthu amagwiritsa ntchito tsamba linalake kapena chakudya pochitira munthu wina zamatsenga. Iwo amatenga chakudya kapena tsambalo n’kupatsa mtsikana kuti iye azikopa amuna. Komabe zimenezi n’zosiyana ndi zimene zingachitike ngati mtsikana wachita kupatsidwa mankhwala ogonetsa tulo iye asakudziwa, kenako n’kumugwiririra. Zikatero, ndiye kuti mtsikanayo amakhala wosalakwa.