Mawu a M'munsi
a Atayenda ulendo wochokera ku Iguputo, Aisiraeli anali okonzeka kulowa m’dziko la Kanani, limene Mulungu analonjeza Abulahamu. Koma azondi 10 atabweretsa lipoti loipa, anthuwo anayamba kung’ung’udza pom’dandaula Mose. Choncho, Yehova ananena kuti Aisiraeli akhale m’chipululumo kwa zaka 40 n’cholinga choti anthu onse ong’ung’udzawo afere m’chipululumo.