Mawu a M'munsi
c M’nthawi ya Yesu Khristu ndi atumwi ake, mabuku onse a Malemba Achiheberi anali atawamasulira m’Chigiriki. Mabuku amenewa anayamba kutchedwa Baibulo la Septuagint ndipo Ayuda olankhula Chigiriki ankakonda kuligwiritsa ntchito kwambiri. Mavesi ambiri a m’Malemba Achiheberi amene ali m’Malemba Achigiriki Achikhristu anatengedwa m’Baibulo la Septuagint.