Mawu a M'munsi
b Vuto linanso lokhudza mabuku owonjezerawa ndi lakuti amene alipo ndi ochepa kwambiri. Mwachitsanzo, mbali ya buku la Uthenga Wabwino wa Mariya Mmagadala imene idakalipo, ndi mipukutu iwiri ing’onoing’ono ndiponso mpukutu umodzi wokulirapo umene uli ndi theka lokha la mawu amene analembedwa poyambirira. Komanso, zimene zinalembedwa m’mipukutu imene ilipoyi zimasiyana kwambiri.