Mawu a M'munsi
a Kalelo anthu ankakonda kupha nkhosa pofuna kusonyeza mlendo kuti amulandira ndi manja awiri. Koma kuba nkhosa ya wina unali mlandu womwe chilango chake chinali kubweza nkhosa zinayi. (Eksodo 22:1) Davide anaona kuti munthu wolemerayo sanasonyeze chifundo potenga nkhosa ya munthu wosaukayo. Pochita zimenezi iye analanda wosaukayo nkhosa imene ikanathandiza banja lake kupeza mkaka ndi ubweya, mwinanso akanaisunga kuti idzabereke nkhosa zina.